Genesis 23:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Abrahamu adaika mkazi wake Sara m'phanga la munda wa ku Makipera kuvuma kwa Mamure, (ndiye kuti Hebroni), m'dziko la Kanani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zitatha izi Abrahamu anaika Sara mkazi wake m'phanga la munda wa Makipela patsogolo pa Mamure (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitatha izi, Abrahamu anayika mkazi wake Sara mʼphanga la mʼmunda wa ku Makipela, kufupi ndi ku Mamre (kumene ndi ku Hebroni) mʼdziko la Kanaani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zitatha izi Abrahamu anaika Sara mkazi wace m'phanga la munda wa Makipela patsogolo pa Mamre (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani.