Genesis 23:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo adafera ku Kiriyati-Ariba (ndiye kuti Hebroni) m'dziko la Kanani. Abrahamu adapita kumeneko nakalira maliro a Sarayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Sara anafa m'Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anamwalirira ku Kiriyati-Araba, kumeneku ndi ku Hebroni, mʼdziko la Kanaani, ndipo Abrahamu anapita kukakhuza maliro a Sara, namulirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sara anafa m'Kiriyati-araba (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.