Genesis 23:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
naŵauza kuti, “Ngati mukuvomera kuti ndiike mkazi wangayu kuno, chonde pemphereni Efuroni Muhiti, mwana wa Zohari,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena nao, kuti, Ngati mukandivomereza kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso, mundimvere ine, mundinenere ine kwa Efuroni mwana wake wa Zohari,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nati, “Ngati mwaloladi kuti ndiyike mkazi wanga kuno, ndiye ndimvereni. Mundipemphere kwa Efroni mwana wa Zohari
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena nao, kuti, Ngati mukandibvomereza kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso, mundimvere ine, mundinenere ine kwa Efroni mwana wace wa Zohari,