Genesis 23:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kuti andigulitse phanga la Makipera ali naloli. Phangalo lili m'malire a munda wake. Mpempheni kuti andigulitse pa mtengo wake ndithu, inu mukupenya, kuti malowo ndiŵasandutse manda.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene lili pansonga pa munda wake; pa mtengo wake wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nao manda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuti andigulitse phanga la Makipela, limene lili kumapeto kwa munda wake. Mumupemphe kuti andigulitse pamtengo wake ndithu inu mukuona kuti akhale manda.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene liri pansonga pa munda wace; pa mtengo wace wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nao manda.