Genesis 24:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika, adazigwaditsa pansi ngamirazo pafupi ndi chitsime, kunja kwa mzinda. Anali madzulo ndithu, nthaŵi imene akazi ankabwera kuchitsimeko kudzatunga madzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anagwaditsa ngamira zake kunja kwa mudzi, ku chitsime cha madzi nthawi yamadzulo, nthawi yotuluka akazi kudzatunga madzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika, anagwaditsa pansi ngamira zija pafupi ndi chitsime chimene chinali kunja kwa mzinda uja. Awa anali madzulo ndithu, nthawi imene amayi amapita kukatunga madzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anagwaditsa ngamila zace kunja kwa mudzi, ku citsime ca madzi nthawi yamadzulo, nthawi yoturuka akazi kudzatunga madzi.