Genesis 24:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndipempha namwali wina kuti, ‘Chonde tatsitsa mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono namwaliyo akandilola kuti, ‘Imwani, ndipo ndikumwetserani ngamira zanu,’ ameneyo ndiye akhale namwali amene mwasankhira mtumiki wanu Isaki. Zimenezi zikachitika, ndidziŵadi kuti mwamkomera mtima mbuyanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamira zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isaki; ndipo chotero ndidzadziwa kuti mwamchitira mbuyanga ufulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndipempha mtsikana wina kuti, ‘Chonde tula mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono iye akayankha kuti ‘Imwani,’ ndipo ndidzapatsanso ngamira zanu madziwo, ameneyo akhale mkazi amene mwasankhira mtumiki wanu Isake.” Zimenezi zikachitika, ndidzadziwa kuti mwaonetsadi kukoma mtima kwanu kosasinthika kwa mbuye wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isake; ndipo cotero ndidzadziwa kuti mwamcitira mbuyanga ufulu.