Genesis 24:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asanamalize nkomwe kupemphera, anangoona uyu, watulukira Rebeka, atasenza mtsuko pa phewa. Iyeyu anali mwana wa Betuele, mwana wa Milika, mkazi wa Nahori, mbale wake wa Abrahamu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asanatsirize kupemphera, anangoona Rebeka watulukira atasenza mtsuko wake pa phewa. Iyeyu anali mwana wa Betueli mwana wa Milika, mkazi wa Nahori mʼbale wake wa Abrahamu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anaturuka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwace wa Abrahamu, ndi mtsuko wace paphewa pace.