Genesis 24:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina adauza wantchito wake wamkulu amene ankayang'anira zinthu zake zonse kuti, “Tandigwira m'kati mwa ntchafu zangamu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wake wamkulu wa pa nyumba yake, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina Abrahamu anawuza wantchito wake wamkulu amene ankayangʼanira zonse anali nazo, kuti “Ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wace wamkuru wa pa nyumba yace, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ncafu yanga: