Genesis 24:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene wasunga mokhulupirika lonjezo lake kwa mbuyanga. Chauta wandilondolera ine ku nyumba ya mbale wake wa mbuyanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m'njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nati, “Alemekezeke Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, amene waonetsa kukoma mtima kwake kosasintha ndi kukhulupirika kwake kwa mbuye wanga. Yehova wanditsogolera pa ulendo wanga mpaka ndafika ku nyumba kwa abale ake a mbuye wanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamuamene sanasiya mbuyanga wopanda cifundo cace ndi zoona zace: koma ine Yehova Wanditsogolera m'njira ya ku nyumba ya abale ace a mbuyanga.