Genesis 24:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamva mlongo wake akusimba zimene munthu uja adaamuuza, Labaniyo adathamangira kuchitsime kumene kunali munthuko. Adakafika pamalo pomwe adaaima wantchito wa Abrahamu, pafupi ndi ngamira zija kuchitsimeko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali, pamene anaona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wake, pamene anamva mau a Rebeka mlongo wake, akuti, Chotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; taonani, anaimirira pa ngamira pakasupe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyeyu atangoona chipini pa mphuno ndi zibangiri pa mikono ya mlongo wake komanso kumva zimene mlendo uja ananena kwa Rebekayo, anathamangira kwa mlendo uja, ndipo anamupeza atangoyima ndi ngamira zake pafupi ndi chitsime.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali, pamene anaona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wace, pamene anamva mau a Rebeka mlongo wace, akuti, Cotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; taonani, anaimirira pa ngamila pakasupe.