Genesis 24:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero munthu uja adakaloŵa m'nyumba, ndipo Labani adamasula katundu amene zidaasenza ngamirazo. Atatero adazipatsa chakudya, naŵapatsa madzi alendo onsewo kuti asambe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthuyo ndipo analowa m'nyumba, namasula ngamira, napatsa ngamira udzu ndi chakudya, ndi madzi akusamba mapazi ake ndi mapazi a iwo amene anali naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho munthu uja analowa mʼnyumba. Labani anatsitsa katundu anali pa ngamira uja. Kenaka anazipatsa ngamira zija chakudya, ndiponso anapereka madzi wosamba mapazi kwa mlendo uja ndi anthu ena onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthuyo ndipo analowa m'nyumba, namasula ngamila, napatsa ngamila maudzu ndi cakudya, ndi madzi akusamba mapazi ace ndi mapazi a iwo amene anali naye.