Genesis 24:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chitabwera chakudya, munthu uja adati, “Sindidya konse mpaka nditanena zimene ndadzera.” Apo Labani adamuuza kuti, “Nenani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaika chakudya pamaso pake: koma anati, Sindidzadya ndisananene chimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chakudya chitabwera mlendo uja anati, “Sindidya mpaka nditakuwuzani zimene ndadzera kuno.” Labani anati, “Yankhulani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaika cakudya pamaso pace: koma anati, Sindidzadya ndisananene cimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu.