Genesis 24:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adamdalitsa kwambiri mbuyanga, ndipo adamkuza kwambiri. Ali ndi nkhosa ndi mbuzi ndi ng'ombe zochuluka. Alinso ndi siliva ndi golide, akapolo aamuna ndi aakazi, ndiponso ngamira ndi abulu ambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo analemera kwakulukulu; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng'ombe, ndi siliva ndi golide, ndi akapolo ndi adzakazi, ndi ngamira ndi abulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova wadalitsa mbuye wanga kwambiri, ndiponso walemera. Wamupatsa nkhosa ndi ngʼombe, siliva ndi golide, antchito aamuna ndi antchito aakazi, komanso ngamira ndi abulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo anakula kwakukuru; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng'ombe, ndi siliva ndi golidi, ndi akapolo ndi adzakazi, oeli ngamila ndi aburu.