Genesis 24:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adandiyankha kuti, ‘Chauta amene ndakhala ndikumumvera nthaŵi zonse, adzatuma mngelo wake kuti apite pamodzi nawe, ndipo adzakuthandiza. Udzampezera mkazi mwana wanga pakati pa anthu anga, m'banja la bambo wanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pake, adzatumiza mthenga wake pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m'njira yako; ndipo ukamtengere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi kunyumba ya atate wanga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iye anayankha, ‘Yehova amene ndakhala ndikumumvera nthawi zonse, adzatumiza mngelo wake kuti akuperekeze ndipo adzakuthandiza mpaka ukamupezere mwana wanga mkazi kuchokera ku mtundu wanga, wa fuko langa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pace, adzatumiza mthenga wace pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m'njira yako; ndipo ukamteogere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi ku nyumba ya atate wanga;