Genesis 24:45 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndisanamalize nkomwe pemphero langalo, ndinangoona uyu, watulukira Rebeka, atasenza mtsuko pa phewa, akutsikira ku chitsime kudzatunga madzi. Tsono ndinampempha kuti, ‘Chonde patseko madzi ndimwe.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndisanathe kunena m'mtima mwanga, taonani, Rebeka anatuluka ndi mtsuko wake pa phewa lake, natsikira ku kasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndisanatsirize kupemphera, ndinangoona Rebeka akutulukira mtsuko wake uli pa phewa. Anatsetserekera ku chitsime kukatunga madzi ndipo ndinati kwa iye, ‘Chonde patseko madzi akumwa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndisanathe kunena m'mtima mwanga, taonani, Rebeka anaturuka ndi mtsuko wace pa phewa lace, natsikira kukasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu.