Genesis 24:47 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye ndinamufunsa kuti, ‘Atate ako ndani?’ Iye anandiyankha kuti, ‘Atate anga ndi Betuele, mwana wa Nahori, amene adamubalira Milika.’ Pamenepo ndinamuveka chipini pa mphuno, ndiponso zigwinjiri pa mikono.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinamfunsa iye kuti, Ndiwe mwana wa yani kodi? Ndipo anati, Ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori amene anambalira iye Milika: ndipo ndinaika mphete pambuyo pake ndi zingwinjiri pa manja ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndinamufunsa kuti, ‘Ndiwe mwana wa yani?’ “Iye anati, ‘Ndine mwana wa Betueli mwana wa Nahori, amene Milika anamuberekera.’ “Tsono ndinayika chipini pa mphuno yake ndi kumveka zibangiri mʼmikono yake,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinamfunsa iye kuti, Ndiwe mwana wa yani kodi? Ndipo anati, Ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori amene anambalira iye Milika: ndipo ndinaika mphete pamphuno pace ndi zingwinjiri pa manja ace.