Genesis 24:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma wantchitoyo adafunsa kuti, “Nanga zidzatani mkaziyo akadzakana kubwera nane kuno? Kodi mwana wanuyo ndidzamperekeze ku dziko lanu kumene mudachokera?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu ku dziko komwe mwachokera inu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wantchito uja anafunsa kuti, “Nanga atakhala kuti mkaziyo sakufuna kubwera nane kuno? Kodi ine ndingadzatenge mwana wanu ndi kubwerera naye ku dziko kumene munachokera?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu kudziko komwe mwacokera inu?