Genesis 24:54 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wantchitoyo pamodzi ndi anthu amene anali nayewo adadya ndi kumwa, ndipo adagona komweko. Atadzuka m'maŵa, mlendoyo adati, “Loleni ndizibwerera kwa mbuyanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadya namwa iye ndi anthu amene anali pamodzi naye, nagonapo usiku: ndipo anauka m'mamawa, ndipo iye anati, Mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono wantchito uja ndi anthu amene anali naye anadya, kumwa nagona komweko. Kutacha mmawa wake, wantchito uja anati, “Mundilole ndibwerere kwa mbuye wanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadya namwa iye ndi anthu amene anali pamodzi naye, nagonapo usiku: ndipo anauka m'mamawa, ndipo iye anati, Mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.