Genesis 24:55 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mai wake wa Rebeka, pamodzi ndi mlongo wakeyo, adati, “Ai, namwaliyu akhale ndi ife kuno kanthaŵi, osachepera masiku khumi, pambuyo pake ndiye adzapite.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mlongo wake ndi amake anati, Namwali akhale ndi ife masiku akuwerengeka, afikire khumi; patsogolo pake iye adzamuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mlongo wake ndi amayi ake a Rebeka anayankha kuti, “Muloleni mtsikanayu abakhala nafe masiku khumi kapena kupyolerapo, kenaka mukhoza kupita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mlongo wace ndi amace anati, Namwali akhale ndi ife masiku akuwerengeka, afikire khumi; patsogolo pace iye adzamuka.