Genesis 24:60 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adamdalitsa Rebekayo ponena mau akuti, “Iwe mwana wathu, Chauta akudalitse kuti udzakhale mai wa anthu zikwi zambirimbiri. Zidzukulu zako zidzagonjetse mizinda ya adani ao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iwo anadalitsa Rebeka ndi kumuwuza kuti, “Iwe ndiwe mlongo wathu, Mulungu akudalitse iwe, ukhale mayi wa anthu miyandamiyanda; ndi kuti zidzukulu zako zidzalanda mizinda ya adani awo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse cipata ca iwo akudana nao.