Genesis 24:65 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
nafunsa wantchitoyo kuti, “Nanga munthu ali akudza kunoyu ndani?” Wantchito uja adayankha kuti, “Ndiye mbuyanga uja ameneyu.” Motero Rebeka adatenga nsalu, nadziphimba kumaso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa mnyamata, Munthuyo ndani amene ayenda m'munda kukomana ndi ife? Mnyamatayo ndipo anati, Uyo ndi mbuyanga: chifukwa chake namwali anatenga chophimba chake nadziphimba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nafunsa wantchito uja kuti, “Kodi munthu uyo ndi ndani akuyenda mʼmundamo kubwera kudzakumana nafe?” Wantchitoyo anayankha, “Ndiye mbuye wanga.” Choncho Rebeka anatenga nsalu ndi kufunda kumaso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa mnyamata, Munthuyo ndani amene ayenda m'munda kukomana ndi ife? Mnyamatayo ndipo anati, Uyo ndi mbuyanga: cifukwa cace namwali anatenga cophimba cace nadziphimba.