Genesis 24:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu Wakumwamba, adanditenga kwathu m'banja mwa bambo wanga ndi m'dziko limene ndidabadwira, ndipo adandilonjeza molumbira kuti, ‘Dziko lino ndidzapatsa zidzukulu zako.’ Chautayo adzatuma mngelo wake wokutsogolera, ndipo kumeneko udzamutengera mkazi mwana wanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine kunyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; Iye adzatumiza mthenga wake akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Mulungu wakumwamba amene ananditenga kwa makolo anga nanditulutsa mʼdziko lobadwira, ameneyo anayankhula nane molumbira kuti, ‘Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko ili.’ Iyeyu adzatumiza mngelo wake kuti akutsogolere kumeneko kukapezera mwana wanga mkazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine ku nyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; iye adzatumiza mthenga wace akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.