Genesis 25:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adamuuza kuti, “M'mimba mwako muli mitundu iŵiri ya anthu. Udzabereka mafuko a anthu olimbana: mwana wina adzakhala wamphamvu kupambana mnzake, wamkulu adzakhala wotumikira wamng'ono.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri ili m'mimba mwako, magulu awiri a anthu adzatuluka m'mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati kwa iye, “Udzabala mafuko awiri a anthu olimbana, ndipo magulu awiri a anthu ochokera mwa iwe adzasiyana; fuko limodzi lidzakhala la mphamvu kuposa linzake, ndipo wamkulu adzatumikira wamngʼono.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri iri m'mimba mwako, Magulu awiri a anthu adzaturuka m'mimba mwako; Gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzace; Wamkuru adzakhala kapolo wa wamng'ono.