Genesis 25:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pobadwa mng'ono wake, dzanja lake linali litagwira chidendene cha Esau. Motero adamutcha Yakobe. Pamene ana ameneŵa ankabadwa, nkuti Isaki ali wa zaka 60.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pambuyo pake ndipo anabadwa mphwake ndipo dzanja lake linagwira chitende cha Esau, ndi dzina lake linatchedwa Yakobo: ndipo Isaki anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wake anabala iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mʼbale wake anabadwa atagwira chidendene cha Esau; choncho anamutcha Yakobo. Isake anali ndi zaka 60 pamene Rebeka anabereka mapasawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pambuyo pace ndipo anabadwa mphwace ndipo dzanja lace linagwira citende ca Esau, ndi dzina lace linachedwa Yakobo: ndipo Isake anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wace anabala iwo.