Genesis 25:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yakobe adapatsa Esau buledi pamodzi ndi nyemba zija, ndipo Esau adadya namwera, kenaka adanyamuka nkuchokapo. Motero Esauyo adanyoza ukulu wake wauchisamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yakobo anampatsa Esau mkate ndi mphodza zophika; ndipo iye anadya, namwa, nanyamuka, napita: chomwecho Esau ananyoza ukulu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yakobo anamupatsa Esau buledi ndi phala lofiira lija. Iye anadya ndi kumwa, nanyamuka kumapita. Motero Esau anapeputsa ukulu wake wachisamba uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yakobo anampatsa Esau mkate ndi mphodza zophika; ndipo iye anadya, namwa, nanyamuka, napita; comweco Esau ananyoza ukulu wace.