Genesis 25:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma asanafe adaŵapatsako mphatso ana ake ena aja amene adaŵabereka mwa akazi ake enawo. Onsewo adaŵatumiza ku dziko lakuvuma kuti akakhale kumeneko, kuŵachotsa kwa mwana wake Isaki.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kwa ana a akazi ake ang'ono amene Abrahamu anali nao Abrahamu anapatsa mphatso, nawachotsa iwo kwa Isaki mwana wake, akali ndi moyo, kuti anke kum'mawa, ku dziko la kum'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene anali ndi moyo, Abrahamu anapereka mphatso kwa ana aakazi ake ena onse. Kenaka anawatumiza ku dziko la kummawa kuti akhale kutali ndi mwana wake Isake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kwa ana a akazi ace ang'ono amene Abrahamu anali nao Abrahamu anapatsa mphatso, nawacotsa iwo kwa Isake mwana wace, akali ndi moyo, kuti anke kum'mawa, ku dziko la kum'mawa.