Genesis 25:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana ake aja, Isaki ndi Ismaele, adamuika m'phanga lija la Makipera, m'munda umene kale udaali wa Efuroni mwana wa Zohari wa ku Hiti. Mundawo unali chakuvuma kwa Mamure.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana ake Isaki ndi Ismaele anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efuroni mwana wake wa Zohari Muhiti, umene uli patsogolo pa Mamure;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana ake, Isake ndi Ismaeli anamuyika mʼphanga la Makipela pafupi ndi Mamre, mʼmunda umene kale unali wa Efroni mwana wa Zohari Mhiti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana ace Isake ndi Ismayeli anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efroni mwana wace wa Zohari Mhiti, umene uli patsogolo pa Mamre;