Genesis 26:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abimeleki adamufunsa kuti, “Bwanji iwe wachita zotere? Wina mwa anthu angaŵa bwenzi atamfunsira mkazi wako, iweyo ukadatichimwitsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abimeleki anati, Nchiyani chimenechi watichitira ife? Panatsala pang'ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadatichimwitsa ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Abimeleki anati, “Nʼchiyani chimene watichitira? Mmodzi mwa anthuwa anatsala pangʼono kugona ndi mkazi wako ndipo ukanatisandutsa ife kukhala olakwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abimeleke anati, Nciani cimeneci waticitira ife? panatsala pang'ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadaticimwitsa ife: