Genesis 26:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Abimeleki adalamula anthu ake onse kuti, “Musamuchite kanthu munthuyu pamodzi ndi mkazi wake yemwe. Wina aliyense akangotero, aphedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abimeleki anauza anthu ake, nati, Aliyense amene akhudza mwamuna uyo kapena mkazi wake, zoonatu adzaphedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Abimeleki analamula anthu ake onse nati, “Aliyense amene avutitse munthu uyu pamodzi ndi mkazi wake adzaphedwa ndithu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abimeleke anauza anthu ace, nati, Ali yense amene akhudza mwamuna uyo kapena mkazi wace, zoonatu adzaphedwa.