Genesis 26:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Afilisti adayamba kuchita naye kaduka, chifukwa choti anali ndi nkhosa ndi ng'ombe zambiri, pamodzi ndi akapolo ochuluka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo anali ndi chuma cha nkhosa, ndi chuma cha zoweta, ndi banja lalikulu: ndipo Afilisti anamchitira iye nsanje.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anali ndi nkhosa, ngʼombe ndi antchito ambiri mwakuti Afilisti anamuchitira nsanje.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo anali ndi cuma ca nkhosa, ndi cuma ca zoweta, ndi banja lalikuru: ndipo Afilisti anamcitira iye nsanje.