Genesis 26:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adachoka kumeneko, nakakumba chitsime china. Pa chimenechi panalibe mkangano, motero adachitcha Ufulu. Adati, “Tsopano Chauta watipatsa ufulu m'dziko, ndipo tidzalemera kuno.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachoka kumeneko nakumba chitsime china; koma sanakangane nacho chimenecho; ndipo anatcha dzina lake Rehoboti; ndipo anati, Chifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m'dziko muno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anachokapo pamenepo nakakumba china. Koma apa sanakanganiranenso ndi munthu. Iye anachitcha Kutakasuka, nati, “Tsopano Yehova watipatsa ife malo otakasukirako ndipo tilemera muno.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacoka kumeneko nakumba citsime cina; koma sanakangana naco cimeneco; ndipo anacha dzina lace Rehoboti; ndipo anati, Cifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m'dziko muno.