Genesis 26:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khala kuno ndipo Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakudalitsa chifukwa ndidzapereka maiko onseŵa kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako. Ndidzasunga lumbiro limene ndidachita kwa bambo wako Abrahamu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa chilumbiriro ndinachilumbirira kwa Abrahamu atate wako;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Khala mʼdziko lino ndipo ndidzakhala nawe ndi kukudalitsa. Pakuti kwa iwe ndi zidzukulu zako ndidzapereka mayiko onsewa. Choncho ndidzakwaniritsa pangano limene ndinalumbira kwa Abrahamu, abambo ako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe cifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa cilumbiriro ndinacilumbirira kwa Abrahamu atate wako;