Genesis 26:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, adakwatira Yuditi mwana wa Beeri Muhiti. Adakwatiranso Basemati, mwana wa Eloni Muhiti.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Muhiti, ndi Basemati mwana wamkazi wa Eloni Muhiti:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Esau anali ndi zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Mhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa mkazi wa Eloni Mhiti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Mhiti, ndi Basemati mwana wamkazi wa Elone Mhiti: