Genesis 26:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu akumeneko atafunsa za mkazi wake, Isaki adati, “Ameneyu ndi mlongo wanga.” Ankachita mantha kunena kuti, “Ndi mkazi wanga.” Ankaopa kuti anthu akumenekowo angamuphe ndipo angakwatire Rebeka, popeza kuti anali wokongola kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wake; ndipo iye anati, Ndiye mlongo wanga: chifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine chifukwa cha Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu akumaloko atafunsa Isake za mkazi wake, iye anati, “Ndi mlongo wanga ameneyu.” Iye anaopa kunena kuti, “Ndi mkazi wanga ameneyu,” popeza ankaganiza kuti anthu akumeneku akhoza kumupha ndi kukwatira mkazi wake popeza Rebeka anali wokongola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wace; ndipo iye anati, diye mlongowanga: cifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine cifukwa ca Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.