Genesis 26:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Isaki atakhala kumeneko kanthaŵi ndithu, Abimeleki mfumu ya Afilisti adasuzumira pa zenera kuyang'ana kunja, naona Isaki atakumbatira Rebeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anayang'ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isaki analinkuseka ndi Rebeka mkazi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Isake atakhalako kumeneko nthawi yayitali, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anasuzumira pa zenera kuyangʼana kunja, ndipo anaona Isake akugwiragwira Rebeka, mkazi wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleke mfumu ya Afilisti, anayang'ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isake analinkuseka ndi Rebeka mkazi wace.