Genesis 26:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Abimeleki adatuma munthu kukaitana Isaki. Ndipo adati, “Ameneyu ndi mkazi wako ndithu. Bwanji mujamu unkanena kuti ndi mlongo wako?” Iye adayankha kuti, “Ndinkaganiza kuti ndidzaphedwa ndikanena kuti ndi mkazi wanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abimeleki anamuitana Isaki nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isaki anati kwa iye, Chifukwa ndinati, Ndingafe chifukwa cha iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Abimeleki anamuyitanitsa Isake nati, “Uyu ndi mkazi wako ndithu! Nanga bwanji umati, ‘Ndi mlongo wanga’?” Ndipo Isake anamuyankha kuti, “Ine ndimaganiza kuti ndingataye moyo wanga chifukwa cha iyeyu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abimeleke anamuitana Isake nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isake anati kwa iye, Cifukwa ndinati, Ndingafe cifukwa ca iye.