Genesis 27:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yakobe adauza mai wake kuti, “Mukudziŵa kuti Esau ndi wacheya, koma ine khungu langa ndi losalala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amake, Taonani, Esau mkulu wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu wosalala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yakobo anati kwa Rebeka amayi ake, “Komatu mʼbale wanga Esau ndi munthu wa khungu la ubweya zedi, ndipo ine ndine munthu wa khungu losalala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amace, Taonani, Esau mkuru wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu, wosalala.