Genesis 27:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sadamzindikire Yakobe popeza kuti mikono yake inali yacheya ngati ya Esau. Motero adayambapo kumdalitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sanamzindikire iye, chifukwa kuti manja ake anali aubweya, onga manja a Esau mkulu wake; ndipo anamdalitsa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sanamuzindikire, popeza mikono yake inali ndi ubweya ngati ya mʼbale wake Esau; choncho anamudalitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sanazindikira iye, cifukwa kuti manja ace anali aubweya, onga manja a Esau mkuru wace; ndipo anamdalitsa iye.