Genesis 27:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyenso adaphika chakudya chabwino kwambiri, nakapereka kwa bambo wake. Esauyo adati, “Chonde bambo dzukani, khalani tsonga, mudye nyama imene ine mwana wanu ndakutengerani, ndipo mundidalitse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iyenso anakonza chakudya chokolera, nadza nacho kwa atate wake, nati kwa atate wake, Auke atate wanga, adye nyama ya mwana wake, kuti moyo wanu undidalitse ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nayenso anakonza chakudya chokoma nabwera nacho kwa abambo ake. Ndipo anati kwa iye, “Chonde abambo, dzukani mukhale tsonga kuti mudye nyamayi ndi kuti mundidalitse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iyenso anakonza cakudya cokolera, nadza naco kwa atate wace, nati kwa atate wace, Auke atate wanga, adye nyama ya mwana wace, kuti moyo wanu undidalitse ine.