Genesis 27:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pompo Isaki adayamba kunjenjemera thupi lonse, nafunsa kuti, “Nanga uja adapha nyama nkubwera nayo kwa ineyu ndani? Ndadya kale imeneyo, iwe usanabwere. Ndamudalitsa kale, ndipo madalitso amenewo ndi ake mpaka muyaya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Isaki ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukulu, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadalowe iwe, ndipo ndamdalitsa iye? Inde, adzadalitsika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Isake ananjenjemera kwambiri nati, “Nanga ndani uja anakapha nyama kutchire nʼkudzandipatsa? Ine ndadya kale, ndadya nyamayo iwe utangotsala pangʼono kubwera ndipo ndamudalitsa ndipo adzakhaladi wodalitsika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Isake ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukuru, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadaloweiwe, ndipondamdalitsaiye? inde, adzadalitsika.