Genesis 27:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Isaki adayankha Esauyo kuti, “Ndamudalitsa kale iyeyo kuti akhale mbuyako, ndipo abale ake onse ndaŵasandutsa atumiki ake. Ndampatsa chakudya ndi chomwera chake. Nanga tsopano chatsalanso nchiyani choti ndikuchitire iwe mwana wanga?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayankha Isaki nati kwa Esau, Taona, ndamuyesa iye mkulu wako, ndi abale ake onse ndampatsa iye akhale akapolo ake; ndakhazikitsa iye ndi tirigu ndi vinyo; nanga pamenepo mwana wanga, ndidzakuchitira iwe chiyani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Isake anamuyankha nati, “Ndamudalitsa iye kuti akhale wokulamulira iwe. Ndaperekanso abale ake onse kuti akhale omutumikira iye, ndipo ndamudalitsa ndi tirigu wambiri, ndi vinyo watsopano. Ndiye ndingakuchitirenso chiyani mwana wanga?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayankha Isake nati kwa Esau, paona, ndamuyesa iye mkuru wako, ndi abale ace onse ndampatsa iye akhale akapolo ace; ndakhazikitsa iye ndi tirigu ndi vinyo; nanga pamenepo mwana wanga, ndidzakucitira iwe ciani?