Genesis 27:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ntchito yako idzakhala yomenya nkhondo, ndipo udzakhala wotumikira mbale wako. Koma ukadzatha kudzimasula, udzachokeratu m'goli la ulamuliro wake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wa mphwako. Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka, udzachotsa goli lake pakhosi pako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzakhala ndi moyo podalira lupanga ndipo udzatumikira mʼbale wako. Koma idzafika nthawi pamene udzakhala mfulu udzachotsa goli lake mʼkhosi mwako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wamphwako; Ndipo padzakhalapamene udzapulumuka, Udzacotsa gori lace pakhosi pako.