Genesis 27:42 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Rebeka atamva za maganizo onse a Esau, adaitana Yakobe namuuza kuti, “Taona, mbale wako Esau akuganiza zoti akuphe kuti akulipsire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anauza Rebeka mau a Esau mwana wake wamkulu: ndipo iye anatumiza naitana Yakobo mwana wake wamng'ono, nati kwa iye, Taona, mkulu wako Esau, kunena za iwe, adzitonthoza yekha mtima wake kuti adzakupha iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Rebeka anamva zimene mwana wake wamkulu Esau ankaganiza, anayitanitsa Yakobo nati kwa iye, “Mʼbale wako Esau akulingalira zakuti akuphe kuti akulipsire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anauza Rebeka mau a Esau mwana wace wamkuru: ndipo iye anatumiza naitana Yakobo mwana wace wamng'ono, nati kwa iye, Taona, mkuru wako Esau, kunena za iwe, adzitonthoza yekha mtima wace kuti adzakupha iwe.