Genesis 27:45 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mpaka mtima wa mbale wako utatsika ndi kuiŵala zonse zimene wamchitazi. Pa nthaŵiyo, ine ndidzatuma munthu kudzakutenga. Nanga nditayirenji inu ana anga aŵiri pa tsiku limodzi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mpaka wakuchokera mkwiyo wa mkulu wako, kuti aiwale chimene wamchitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse awiri tsiku limodzi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mkwiyo wa mʼbale wakoyo ukadzatsika ndi kuyiwala zonse wamuchitirazi, ndidzatuma munthu kuti adzakutenge. Nanga nditayirenji nonse awiri nthawi imodzi?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mpaka wakucokera mkwiyo wa mkuru wako, kuti aiwale cimene wamcitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse awiri tsiku limodzi?