Genesis 28:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika pamalo pena, adaima pamenepo chifukwa dzuŵa linali litaloŵa. Adagona pompo atatsamira mwala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafika kumalo, nagona kumeneko usiku, chifukwa lidalowa dzuwa: ndipo anatenga mwala wa kumeneko, nauika pansi pa mutu wake, nagona tulo kumeneko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika pa malo pena, anayima kuti agonepo chifukwa dzuwa linali litalowa. Anatenga mwala wina pomwepo natsamiritsapo mutu wake, ndipo anagona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafika kumalo, nagona kumeneko usiku, cifukwa lidalowa dzuwa: ndipo anatenga mwala wa kumeneko, nauika pansi pa mutu wace, nagona tulo kumeneko.