Genesis 28:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndili nawe, ndidzakutchinjiriza kulikonse kumene udzapite, ndipo ndidzakubwezanso ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zonse ndakuuzazi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndili nawe pamodzi ndipo ndidzakuyangʼanira kulikonse upiteko, ndipo ndidzakubwezera ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zimene ndakulonjezazi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, Ine ndiri pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; cifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditacita cimene ndanena nawe.