Genesis 28:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatero Isaki adatumiza Yakobe ku Mesopotamiya kwa Labani, mwana wa Betuele Mwaramu. Labani anali mlongo wa Rebeka mai wa Yakobe ndi Esau.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Isaki anamlola Yakobo amuke, ndipo ananka ku Padanaramu kwa Labani, mwana wake wa Betuele Mwaramu, mlongo wake wa Rebeka, amai wao wa Yakobo ndi Esau.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Isake anamulola Yakobo kuti anyamuke kupita ku Padanaramu kwa Labani mwana wa Betueli Mwaramu. Labani anali mlongo wa Rebeka, mayi wa Yakobo ndi Esau.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Isake anamlola Yakobo amuke, ndipo ananka ku Padanaramu kwa Labani, mwana wace wa Betuele Msuriya, mlongo wace wa Rebeka, amai wao wa Yakobo ndi Esau.