Genesis 28:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Esau adamva kuti Isaki wadalitsa Yakobe, ndipo kuti Yakobeyo watumizidwa ku Mesopotamiya kuti akakwatire kumeneko. Adamvanso kuti pomudalitsapo, adamlamula kuti asadzakwatire mkazi wa ku Kanani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaona Esau kuti Isaki anamdalitsa Yakobo namtumiza ku Padanaramu kuti atenge mkazi wa kumeneko; ndiponso kuti pamene anamdalitsa iye, anamuuza iye kuti, Usatenge mkazi wa ana akazi a Kanani;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano Esau anadziwa kuti Isake anadalitsa Yakobo ndi kumutumiza ku Padanaramu kuti akakwatire kumeneko. Anawuzidwanso kuti, “Usakwatire mkazi wa ku Kanaani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaona Esau kuti Isake anamdalitsa Yakobo namtumiza ku Padanaramu kuti atenge mkazi wa kumeneko;