Genesis 28:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adapita kwa Ismaele mwana wa Abrahamu, nakwatira Maharati mwana wa Ismaele, mlongo wa Nebayoti.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo Esau ananka kwa Ismaele, naonjezera kwa akazi amene anali nao, natenga Mahalati mwana wamkazi wa Ismaele mwana wa Abrahamu, mlongo wake wa Nebayoti akhale mkazi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
anapita kwa Ismaeli mwana wa Abrahamu nakwatira Mahalati mwana wa Ismaeli, mlongo wake wa Nebayoti. Anatero kuwonjezera akazi amene anali nawo kale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ananka kwa Ismayeli, naonjezera kwa akazi amene anali nao, natenga Mahalati mwana wamkazi wa Ismayeli mwana wa Abrahamu, mlongo wace wa Nebayoti akhalemkazi wace.