Genesis 29:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yakobe ataona Rakele ali ndi nkhosa za bambo wake Labani, adapita kuchitsimeko, nakunkhuniza mwalawo, nkuzimwetsa madzi nkhosa za Labanizo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali pamene Yakobo anaona Rakele, mwana wamkazi wa Labani, mlongo wake wa amake, ndi nkhosa za Labani mlongo wake wa amake, Yakobo anayandikira nagubuduza kuuchotsa mwala pachitsime, nazimwetsa zoweta za Labani, mlongo wake wa amake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yakobo ataona Rakele mwana wa Labani, mlongo wa amayi ake, ali ndi nkhosa za Labani, anapita nawugudubuza mwala uja nazimwetsa madzi nkhosa za amalume akezo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali pamene Yakobo anaona Rakele, mwana wamkazi wa Labani, mlongo wace wa amace, ndi nkhosa za Labani mlongo wace wa amace, Yakobo anayandikira nagubuduza kuucotsa mwala pacitsime, nazimwetsa zoweta za Labani, mlongo wace wa amace.